A Songwe anena izi lolemba pomwe anakonza mkumano wa adindo osiyanasiyana kuphatikizapo mafumu ndicholinga chowafotokozera zomwe achita kuchokera mchaka cha 2019.
“Munthawi yomwe ndakhala ndikukutumikilani ndakumana ndi zokhoma monga, kufowoka kwa akomiti oyang’anila ma polojekiti akudera, ma komiti a VDC ndi ADC kusalondoloza zitukuko, khonsolo kugula zipangizo zosayenera komanso kuchedwa kuyamba ntchito mwazina” anatero a Songwe.
Komabe phunguyu wati wakwanitsa ena mwa malonjezo ake mwachitsanzo, kubweletsa bwalo lamilandu, kuthetsa mavuto amagetsi, kumaliza zitukuko zimene zinayambidwa kale komanso kukhazikitsa thumba la ndalama zothandizila ana ovutika mu sukulu za sekondale.
Mkumanowu wachitika pomwe ma udindo a aphungu mdziko lino akhale akutha mwezi wa July chaka chino pokonzekela chisankho chapatatu chomwe chidzachitike pa 16 September.