Masewero omwe anachitikira pa Likoma Community Football ground la lamulungu anabweletsa kwimbi la anthu kuchokera m’madera onse aboma la Likoma ndipo anali masewero apamwamba.
M’mawu ake Mlembi wa mkulu wa bungwe loyendetsa masewero ku Likoma a Kondwani Binga ati chikho cha FAM Under 21 chawonetsa luso lomwe achanyamata achichepere alinalo, Iye watinso apeza kale zikho zina monga Castle Imbongetse, Christopher Ashems Songwe League, komanso FAM CUP zimene zikhale zikuyambanso posachedwapa chaka chino.
Captain wa Chiponde FC Benjamin Khuni wayamika bungweli pa ntchito yomwe akugwira yosaka thandizo kuti masewero ampira adzipita patsogolo m’bomali.
Naye Mike Gondwe yemwe ndi m’modzi mwa atsogoleri a team ya Red Arrows avomeleza kugonja kwawo ndipo ati mpikisano uliwonse amapambana ndi m’modzi.
Ma team okwana 14 ndiwomwe anatenga nawo mbali mu mpikisanowo, ndipo team ya Chiponde yapita ndi ndalama zokwana 1 miliyoni kwacha, pomwe team ya Red Arrows yatenga K400,000, pomwe Madimba yachoka ndi K200,000.
LikomaFM, Online News.