Home Politics Gulu la Taskforce lomwe ndi nthambi ya chipani cha Malawi Congress Party m’boma la Likoma lapeleka Cement kuti amalizile nyumba ya chigayo.

Gulu la Taskforce lomwe ndi nthambi ya chipani cha Malawi Congress Party m’boma la Likoma lapeleka Cement kuti amalizile nyumba ya chigayo.

by Oliver Malibisa
0 comments

Polankhula lachinayi pamwambo opeleka cement ku komiti yoyendetsa chigayochi, a Innocent Aponda omwe ndi mmodzi mwa guluri ati achita chidwi powona momwe phungu wa Likoma a Christopher Ashems Songwe akuchita pa nkhani ya zitukuko pomwe apeleka zigayo ziwiri dera la Chiponde ndi Chinyanya zomwe azigula ndi ndalama za mthumba mwawo.

Mlembi wakomiti ya chigayochi a Edward Chirwa ayamikira guluri kamba kathandizoli ndipo ati akonza kale ndondomeko yakayendetsedwe kantchitoyi ndipo mwazina ndikuzathandiza osowa, kulipilira feez komanso kukonzera zitukuko zina mdelari.

Mfumu yadelari Group Village Headman Mwase yathokoza a Joe Noel Chilala omwe azayimire delari ngati khansala kamba kosaka thandizoli.

Guluri lapereka matumba okwana khumi.

LikomaFM, OnlineNews.

You may also like

Leave a Comment

Likoma (LCR) is a community radio for Likoma District licensed by
Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) in December
2013.The Radio is covering the whole of Likoma District including
Chizumulu, parts of Nkhata Bay,Mzuzu and Nkhotakota. The radio
station enjoys a listenership of about 50,000 comprising of 17,000 from
the island and others from Nkhata Bay, Nkhotakota and some parts
of Mozambique.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00