A Yamikani Mwambafula awuza Likoma Radio kuti pakadali pano chilichonse chokonzekera mwambowu chilimchimake ndipo ati patsikuli anthu ayembekezere kudzasangalatsidwa ndi oyimba osiyanasiyana kuphatikizapo Gibo Piason.
A Mwambafula awonjezera kuti Guest House yi ili ndizipinda zokwana 39 komanso ma charlets 10.
“Ndapanga izi podziwa kuti chilumba cha Likoma ndimbali imodzi yamalo okopela alendo m’dziko lino ndipo ndinaona kut ndithandizile kuchepetsa vuto lamalo ogona alendo”.
Iwo atinso nthawi zina alendo akabwera ochuluka ku Likoma amasowa malo ogona kaamba kakuchepa kwamalo ndipo ati ndichiyembekezo chawo kuti Mwayi Wanga Guest House ichepetsa vutoli.
Malowa omwe amangidwa mwamakono ali ndimalo wodyela komanso malo omwe makasitomala awo adzitha kumaonela mpira ndizina kudzera pa DSTV.
LikomaFM, OnlineNews.