Home Featured Wapampando oyang’anila chitukuko chadera la kumwera kwa chilumba cha Likoma a Anson Putaputa ati akusowekera maphunziro kuti ayambe kugwira ntchito yawo mwaukadaulo.

Wapampando oyang’anila chitukuko chadera la kumwera kwa chilumba cha Likoma a Anson Putaputa ati akusowekera maphunziro kuti ayambe kugwira ntchito yawo mwaukadaulo.

by Chiletso Bisweck
0 comments

A Putaputa anena izi kutsatila zomwe wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo yemwenso ndi phungu wa boma la Likoma a Charles Chilambula anabweza zina mwazitukuko zomwe anthu am’bomali adasankha kudzera kuma Village Development Committee VDC.

“tikulankhulana ndi akukhonsolo cholinga chakuti tiphunzire bwino kenako tikasanthure zitukuko zomwe zichitike pazaka zisanu zikudzazi”, atero a Putaputa.

Masiku apitawa a Chilambula anayitanitsa akomiti oyang’anira zitukuko zakudera kuwakumbutsa kuti pakali pano ndalama ya CDF ndiyochuluka kusiyana ndizaka zam’mbuyomu choncho anthu akudera akuyenera kusankha zitukuko zolingana ndi ndalamayi.

“ena anapempha zigayo ena zimbudzi zam’mbali mwanyanja zomwe asodzi angakwanitse pawokha titayika malamulo apadera”, anatero a Chilambula.

Iwo analangiza nyumbayi kuti 5 billion ikufunika zitukuko zikuluzikulu monga misewu yabwino, kuyika zofunikira mzipatala, kukonza malo otsikira ndi kukwera sitima pa chilumba cha Chizumulu komanso kukonza sukulu za sekondale.

Koma titalankhula ndi mlangizi wa zachitukuko m’bomali a Uledi Mpeta atiuza kuti makomitiwa aphunzitsidwa sabata ino ndithandizo la ndalama zomwe phungu wa Likoma wapeleka koma ati maphunzilowa achitika tsiku limodzi ngakhale amafunika kuti achitike kwa masiku atatu kaamba kakusowa kwa ndalama.

LikomaFM, OnlineNews.

You may also like

Leave a Comment

Likoma (LCR) is a community radio for Likoma District licensed by
Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) in December
2013.The Radio is covering the whole of Likoma District including
Chizumulu, parts of Nkhata Bay,Mzuzu and Nkhotakota. The radio
station enjoys a listenership of about 50,000 comprising of 17,000 from
the island and others from Nkhata Bay, Nkhotakota and some parts
of Mozambique.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00