A Chilambula anena izi lamulungu kutsatila kufika kwa incinerator yi pa chipatala cha Chima m’bomali.
“Kumbuyoku tikafuna kuwotcha zinthu zina tinkazitumiza ku St Gabriel koma tsopano vutoli lichepa”, anena choncho a Chilambula.
Iwo awonjezera kuti tsopano zinthu zidziwotchedwa munthawi yake zomwe zichepetse kufala kwa matenda omwe amadza kudzera mu mpweya oyipa.
Polankhulapo bwana mkubwa wa boma la Likoma Abubakar Nkhoma ayamikira wachiwiri kwa ndunayi pothandizira kuti makinawa afike ku Likoma ndipo ati tsopano ndalama zomwe khonsoloyi inkagwilitsa ntchito powotchera zinyalala kuntunda zidzigwira ntchito zina.
Malingana ndi a Chilambula pakadali pano incinerator ngati imeneyi ili mu mzinda wa Mzuzu ndi boma la Likoma mchigawo cha kumpoto kwa dziko lino.