Home FeaturedFeatured Khothi la first grade magistrate ku Likoma lagamula a Kingsley Lamwele a zaka 18 kukakhala kundende ndikukagwila ntchito yakalavula gaga kwa zaka zinayi kaamba kolowa m’nyumba ndi kuba katundu osiyanasiyana.

Khothi la first grade magistrate ku Likoma lagamula a Kingsley Lamwele a zaka 18 kukakhala kundende ndikukagwila ntchito yakalavula gaga kwa zaka zinayi kaamba kolowa m’nyumba ndi kuba katundu osiyanasiyana.

by Chiletso Bisweck
0 comments

Malingana ndi oyimira boma pa milandu Sub-Inspector Shallnever Mfune adauza khothili kuti usiku wapa 25 July 2026 odandaulayu adatseka nyumba yake koma m’mawa wake anapeza sutikesi ya mdzukulu wake itasowa.

“Sutikesi ndi zinthu zomwe zinali mkati mwake zinali zandalama zokwana 2 million kwacha ndipo zina mwa zinthuzi ndi nsapato, mashati, jazi, mathalauza, yunifolomu za kusukulu, mabulangete komanso 50 sauzande kwacha mwazina”.

First grade magistrate Fordwatch Nyamazana Mkandawire wati wapeleka chilangochi kaamba koti mlandu wakuba katundu wa ophunzira ndi waikulu chifukwa choti umasokoneza maphunziro.

Kingsley Lamwele, amachokera m’mudzi wa Zambala mfumu yaikulu Mwadzama m’boma la Salima.

LikomaFM,OnlineNews.

You may also like

Leave a Comment

Likoma (LCR) is a community radio for Likoma District licensed by
Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) in December
2013.The Radio is covering the whole of Likoma District including
Chizumulu, parts of Nkhata Bay,Mzuzu and Nkhotakota. The radio
station enjoys a listenership of about 50,000 comprising of 17,000 from
the island and others from Nkhata Bay, Nkhotakota and some parts
of Mozambique.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00