M’mawu ake mkulu wamalo ogona alendo a Chiponde Beach Resort a Gedion Khuni ati mwambowu ubweletsa pamodzi anthu ochita malonda osiyanasiyana kuphatikizapo mbeu zomwe zimalimadwa m’bomali.
Iwo atinso pamwambowu padzakakhala kupeleka mphoto komanso kugulitsa zinthu zosiyanasiyana monga tomato, masamba, chinangwa komanso malonda ena pamitengo yotsika kusiyana ndi momwe zimagulitsidwira nthawi zonse.
Mwambo omwe akuutcha kuti Farmers Market, udzachitika pa 1 June 2025, ndipo ukachitikira ku Chiponde Beach Resort pomwe oyimba osiyanasiyana akakometsele mwambowu motsogodzedwa ndi Limban Band.
LikomaFM, OnlineNews.