M’mau ake m’modzi mwa akuluakulu oyang’anila za mayendedwe apa madzi omwe achokera ku nthambi ya Marine, Captain Peter Kajadu ati thandizoli ndilofunika kwambiri m’boma la Likoma komwe njira yokhayo yodalilika ndi yapa madzi.
“Thandizoli lafika mu nthawi yake ndipo ithandizila kupewa ngozi za pa madzi, aliyese akuyenera kukhala ndi udindo ovala chida chozitetezera akamakwera boat kuti zitithandizile kupewa ngozi.” Adatero a Kajadu.
Thandizoli ladza pomwe nduna ya za mtengatenga ndi mtokoma a Jacob Hara atazindikila zovuta zomwe anthu a pa zilumba za Likoma ndi Chizumulu akukumana nazo nthawi yotsika ndi kukwera sitima ngakhaleso nthawi yomwe akwera ma boat kupita kumadera aku mtunda monga Nkhatabay, pomwe ambiri mwa anthuwa amakhala alibe zida zozitetezera pa nthawi yomwe akumana ndi ngozi.
Polandila mphatsoyi yemwe adaimila bwanankubwa wa khonsolo ya Likoma a Wilson Muziya adati thandizoli lafika nthawi yofunikila kwambiri.
“Ngati khonsolo ndife oyamika chifukwa cha thandizoli ndipo tiyesetsa kukhazikitsa malamulo kuti ma life jackets amenewa asamalidwe komaso kugwilitsidwa ntchito yake moyenera.”
Nawo omwe anayimila Senior Chief Mkumpha Mathews Mwera ayamikila kampaniyi komaso boma la Malawi chifukwa choganizila mavuto amene amakhalapo nthawi yokwera kapena kutsika sitima ndipo mfumuyi yapemphaso nzika kuti zisamale komaso kugwilitsa ntchito moyenera katundu yemwe walandilidwayu.
LikomaFM, OnlineNews.
1 comment
https://shorturl.fm/KpmWq