Polankhula lolemba pamwambo opeleka ma computer wa, mkulu woyendetsa ntchito za TEVETA m’chigawo chakumpoto a Joseph Chikopa ati ndicholinga chawo kuti Likoma Community technical college ikhale ndi ana omwe azisulidwa mwaukadaulo kotero apeleka ma Computer wa pofuna kuthandizira ntchito zina zapa sukuluyi
A Joseph apempha khonsolo ya Likoma kuwonetsetsa kuti zipangizozi zakusamalidwa ndicholinga chakuti pomwe mapulani ofuna kukuza sukuluyi ali mkati pasazakhalenso kusowekera zipangizozi.
M’mawu ake wapampando wakhonsoloyi khansala Justina Phiri wayamika bungwe la TEVETA kamba kathandizori, ponena kuti khonsolo payokha sakanatha kupedza ma Computer wa.
“Ndiwonetsetsa kuti katunduyi wapita ku Likoma Community technical college ndipo akugwira ntchito yake moyenera”, atero a Justina.
Likoma Community Technical College inayamba kugwira ntchito zake mchaka cha 2023 ndipo pakadali pano pali phunziro losoka lokha.
LikomaFM,OnlineNews.