Poyankha funso la phungu wa Likoma a Christopher Ashems Songwe lomwe anafunsa lachisanu pa mkumano wa Full Council lokhudza ndondomeko zakalembedwe ka ntchito pakhonsoloyi, a Banabas Sambamo omwe ndi wapampando wa khonsoloyi anati ndizosavuta kulemba ntchito achinyamata ochokera m’bomali chofunika ndikukhala ndizowayeneleza.
A Sambamo anapitiliza kunena kuti posachedwapa akhala akutulutsa chikalata cha mwayi wantchito za Umoyo komanso magawo ena ndipo panthawiyi alankhulana ndi bwana mkubwa wa Likoma kuti achinyamata aku Likoma adzakhale ndi mwayi olembedwa ntchito.
Wayimilira achinyamata ku khonsoloyi Macfallen Mafuta wati ndizoona kuti achinyamata ambiri amakhala kuti zowayeneleza alibe kotero iye wati apita kumakalabu kukalimbikitsana ndi anzake za nkhaniyi.