M,modzi mwa achinyamata omwe apelereka makopewa a Nick Mkuyamba ati cholinga chachikulu cha gulu lawo ndikupititsa patsogolo maphunziro musukulu za primary m’bomali.Nawo a Gresham omweso ndi m’modzi mwa achinyamatawa ati achinyamata ali ndi udindo othandiza pachitukuko chadziko munjira zosiyanasiyana.
“makolo ena kapezedwe kawo ndikovutikila ndichifukwa tinaganiza kuti pomwe sukulu zatsegulira titengepo mbali”.
M’modzi mwa ana opindula Monica Gama wathokoza achinyamatawa ndipo wati thandizoli limuthandizira kuti maphunziro ake ayende bwino.
Achinyamatawa apeleka makope asanu ndi limodzi ndi zolembera ziwiri kwa ana okwana 34.
LikomaFM, OnlineNews.