Polankhula pamsonkhanowu a Mathews Mwela anati anayitanitsa mkumanowu pomwe asodzi ochokera m’maboma ena akupita ku Likoma kukachita usodzi komanso bizinesi, asodziwa akuchokela m’maboma a Mangochi, Salima, Nkhotakota, Kalonga ndi ena, zomwe zikubweletsa umbanda komanso unve ku Likoma.
“asodzi ambiri akubwera osadziwitsa mafumu zomwe zikupeleka chiopsezo ndipo anthu ambili amene akupezeka ndi milandu yakuba kuno ku Likoma ndiwochokela m’maboma ena.”
Senior Chief Mkumpha ati akhala akupangitsa mikumanoyi m’madooko onse, kuti asodzi omwe akuchokela m’maboma ena akhale mkaundula wa amfumu adera lomwe akukhala komanso akhale ndichimbudzi pamalo pomwe akugwilira ntchito yawo.
M’modzi mwa asodzi omwe anachokela m’boma la Mangochi a Piason Nyozani athokoza mfumuyi kaamba kokonza mkumanowu ndipo ati alemekeza ndondomekozi.
Mkumanowu unachitikila pa dooko la mfumu Chalunda komwe anthu ochuluka amafikilako.