Polandila galimotoyi lachinayi m’phunzitsi wamkulu wa pa sukukuyi a Jeremiah Mzumala ati akuthokoza boma kudzera ku nduna yoona za maphunziro a Madalitso Kambauwa Wirima kaamba kokwanilitsa lonjezo lawo.
“anduna azamaphunzilo atabwera pa sukulu yathu mwezi wa epulo chaka chomwechino, tinawadandaulira za vuto la mayendedwe komanso tinawasonyeza galimoto yakale imene tinkakonzetsa pafupipafupi koma simatheka, ndipo kubwera kwa galimoto la tsopanoyi kuchepetsa mavuto ambiri pa sukulu yathu.”
Polankhulapo wapampando wa komiti ya PTA a Anson Putaputa Chirwa anathokoza phungu wa Likoma a Christopher Ashems Songwe poyikapo khama kuti galimotoyi ifike ku Likoma.
“Pakadali pano Budget ichepako kutengela kuti ndalama ina timapeleka kwa akabanza popita kuchipatala ana akadwala, komanso katundu wina tidzithaso kugwiritsa ntchito galimotoyi.” Atero a Putaputa.
LikomaFM,OnlineNews.
11 comments
https://shorturl.fm/ujo7s
https://shorturl.fm/l8POn
https://shorturl.fm/Geqb6
https://shorturl.fm/ByJSm
https://shorturl.fm/ESiwc
https://shorturl.fm/62CsW
https://shorturl.fm/tBEUa
https://shorturl.fm/YWEyn
https://shorturl.fm/4K2Mj
https://shorturl.fm/p72aJ
https://shorturl.fm/akrGI