Madelawa ndi monga, Blantyre, Thyolo, Phalombe, Mangochi, Mwanza, Salima mwa ochepa chabe.
Nthambiyi yati izi zikupereka chiyembekezo cha mvula ya mabingu m’maderawa ndi ena ozungulira m’maola angapo akudzawa. Nthambiyi yati mitambo ya mvulayi ikuyembekezeka kufalikiranso m’madera ena ndipo ati tikhale tcheru chifukwa nyengo itha kusintha nthawi ina iliyonse.
Nyengoyi ikupelekanso ziopsezo za mphenzi ndi mvula ya mphamvu choncho tisabisale pansi pamtengo kukamagwa mvula yamabingu.