Home FeaturedFeatured Wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo yemwenso ndi phungu wa Likoma Islands Constituency olemekezeka a Charles Broomhead Chilambula ati boma ndilodzipereka kupititsa patsogolo ntchito zaumoyo.

Wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo yemwenso ndi phungu wa Likoma Islands Constituency olemekezeka a Charles Broomhead Chilambula ati boma ndilodzipereka kupititsa patsogolo ntchito zaumoyo.

by Chiletso Bisweck
0 comments

A Chilambula amalankhula izi lero pamwambo otsegulira chipatala chaching’ono cha YoMa chomwe chamangidwa m’mudzi wa Yofu m’boma la Likoma.

A Chilambula ati chipatalachi chichepetsa imfa ya ana ang’onoang’ono ndi amayi oyembekezera omwe amafuna thandizo lamsanga komanso chithandizila kuchepetsa matenda.

Polankhulapo wamkulu oyang’anila ntchito za umoyo m’bomali Dr Gracewell Mathewe ati kubwera kwa chipatalachi kusintha zambiri pankhani ya zaumoyo.

“Kutengera ndi level yachipatalachi tidzipereka uphungu kwa amayi oyembekezera, kupereka katemera kwa ana, komanso kuthandiza ngati munthu wavulala mwazina”, atero Dr Mathewe.

Nawo mayi Eneless John ochokera m’mudzi wa mfumu Mnyanje omwe ndiwombekezera pakadali pano ati chipatalachi chichepetsa mtunda omwe amayi oyembekezera amakumana nawo akamapita ku sikelo.

Chipatala cha YoMa chamangidwa ndi ndalama zakwana 146 million kwacha ya thumba la Constituency Development Fund, CDF.

LikomaFM,OnlineNews.

You may also like

Leave a Comment

Likoma (LCR) is a community radio for Likoma District licensed by
Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) in December
2013.The Radio is covering the whole of Likoma District including
Chizumulu, parts of Nkhata Bay,Mzuzu and Nkhotakota. The radio
station enjoys a listenership of about 50,000 comprising of 17,000 from
the island and others from Nkhata Bay, Nkhotakota and some parts
of Mozambique.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00