Home FeaturedFeatured Wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo yemwenso ndi phungu wa Likoma Islands Constituency a Charles Chilambula ati kubwera kwa incinerator m’boma la Likoma kupititsa patsogolo ntchito za umoyo.

Wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo yemwenso ndi phungu wa Likoma Islands Constituency a Charles Chilambula ati kubwera kwa incinerator m’boma la Likoma kupititsa patsogolo ntchito za umoyo.

by Chiletso Bisweck
0 comments

A Chilambula anena izi lamulungu kutsatila kufika kwa incinerator yi pa chipatala cha Chima m’bomali.

“Kumbuyoku tikafuna kuwotcha zinthu zina tinkazitumiza ku St Gabriel koma tsopano vutoli lichepa”, anena choncho a Chilambula.

Iwo awonjezera kuti tsopano zinthu zidziwotchedwa munthawi yake zomwe zichepetse kufala kwa matenda omwe amadza kudzera mu mpweya oyipa.

Polankhulapo bwana mkubwa wa boma la Likoma Abubakar Nkhoma ayamikira wachiwiri kwa ndunayi pothandizira kuti makinawa afike ku Likoma ndipo ati tsopano ndalama zomwe khonsoloyi inkagwilitsa ntchito powotchera zinyalala kuntunda zidzigwira ntchito zina.

Malingana ndi a Chilambula pakadali pano incinerator ngati imeneyi ili mu mzinda wa Mzuzu ndi boma la Likoma mchigawo cha kumpoto kwa dziko lino.

LikomaFM,OnlineNews.

You may also like

Leave a Comment

Likoma (LCR) is a community radio for Likoma District licensed by
Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) in December
2013.The Radio is covering the whole of Likoma District including
Chizumulu, parts of Nkhata Bay,Mzuzu and Nkhotakota. The radio
station enjoys a listenership of about 50,000 comprising of 17,000 from
the island and others from Nkhata Bay, Nkhotakota and some parts
of Mozambique.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00