A Barnabas Sambamu anena izi lamulungu pomwe khonsolo ya Likoma inakonza masewelo ampira wamiyendo ndicholinga chakuti apeleke uthenga wamomwe porogalamuyi imayendela, pamutu wakuti “Mtukula pakhomo kuchepetsa umphawi m’makomo osaukitsitsa”.
“pozindikila kuti anthu amakonda masewela ampila, tinachiwona chopambana kuti tisonkhanitse anthu pamodzi ndicholinga chakuti tiwadziwitse anthu momwe porogalamuyi imayendela, anatero a Sambamo omwenso anali mlendo olemekezeka pamwambowu.
Naye mkulu woyendetsa porogalamuyi m’boma la Likoma a Chritopher Kanaza ati potengera kuti anthu ambiri omwe akupindula mu porogalamuyi pakadali pano ayamba kumene komanso pomwe boma la Likoma layamba kupeleka ndalamazi kudzela pafoni anachiona kuti ndichofunikila kuti apeleke uthengawu panthawi imodzi kutengera ndizokhoma zomwe akukumana nazo.
“sitingakwanitse kupeleka uthengawu khomo ndi khomo ndichifukwa takonza mwambowu kuti tifikile anthu ambiri panthawi yochepa”.
A Kanaza ati mtukula pakhomo imafikila anthu ovutikitsitsa, achikulire, komanso ana amasiye omwe maina awo ali munkhokwe yamaina yomwe imatchedwa UBR pachingelezi.
Naye wachiwili kwa wapampando wa khonsoloyi a Ernest Trever Gulu Banda ati boma limapeleka ndalamazi ndicholinga chakuti opindula adzigula chakudya, kuthandizila ana kusukulu komanso kuchita ma bizinesi ang’ono ang’ono mwazina, kuti akhale odzidalira pachuma ndipo achenjeza opindula kuti atsatile ndondomekozi.
Pamasewelowa timu ya Gunners FC ndiwo akhala akatswili atagonjetsa Red Arrows, ndipo mwambo ngati omwewu unachitikaso pa chilumba cha Likoma loweluka pomwe timu ya Might Islanders inathambitsa timu ya Madimba FC.
LikomaFM, OnlineNews.