Home Featured Bishop wa Anglican Dioceses of Northern Malawi wati mpingo uli ndi udindo waukulu potengapo mbali pachitukuko chadziko lino.

Bishop wa Anglican Dioceses of Northern Malawi wati mpingo uli ndi udindo waukulu potengapo mbali pachitukuko chadziko lino.

by Chiletso Bisweck
10 comments

Rt.Rev. Fanuel Magangani wanena izi lamulungu lapitali pa St Peters Anglican Cathedral m’boma la likoma pamwambo osangalalira kuti Dioceses yi yakwanitsa zaka 30 ikutumikila.

Amagangani anati mpingo ukuyenela kukhala odzidalira pawokha pachuma osati kumangodali maiko akunja. “kale ngakhale zovala za usembe tinkadalira maiko akunja koma pakadali pano takula chifukwa tikudzipangila tokha”.

Ndipo awonjeza kuti pomwe Dioceses yi yakwanitsa zaka 30 ndiwosangalala kuti yakwanitsa kumanga sukulu komanso zipatala mdziko lino.

Nduna yawona za chitetezo cha mdziko a Ezekiel Ching’oma womwe anali mlendo olemekezeka pamwambowu m’malo mwa president wadziko lino anati boma la Dr Lazarus Chakwela limalimbikitsa kuti mipingo idzigwira ntchito limodzi ndi boma pachitukuko ndipo ndiwokondwa kuti mpingowo ukugwila ntchito yotamandika mdziko.

Dr Lazarus Chakwela wathandiza Dioceses yi ndi ndalama zokwana 10,000,000.00 kwacha, pomwe a Ezekiel Ching’oma anapeleka 5,000,000.00.

LikomaFM, Onlinenews.

You may also like

10 comments

Adriana3910 August 6, 2025 - 4:30 pm Reply
Vincent1893 August 8, 2025 - 3:20 pm Reply
Frida1437 August 10, 2025 - 2:37 am Reply
Naomi91 August 10, 2025 - 5:51 pm Reply
Jenny4569 August 13, 2025 - 8:39 am Reply
Samantha3545 August 13, 2025 - 1:14 pm Reply
Andre3040 August 14, 2025 - 10:15 am Reply
Krista4305 August 15, 2025 - 1:23 pm Reply
Harper3530 August 15, 2025 - 8:21 pm Reply
Brielle1086 August 15, 2025 - 11:16 pm Reply

Leave a Reply to Samantha3545 Cancel Reply

Likoma (LCR) is a community radio for Likoma District licensed by
Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) in December
2013.The Radio is covering the whole of Likoma District including
Chizumulu, parts of Nkhata Bay,Mzuzu and Nkhotakota. The radio
station enjoys a listenership of about 50,000 comprising of 17,000 from
the island and others from Nkhata Bay, Nkhotakota and some parts
of Mozambique.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00