Home FeaturedFeatured Pofuna kupititsa patsogolo maphunziro mdziko muno wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo ndi ukhondo yemwenso ndi phungu wa pa zilumba za Likoma ndi Chizumulu wolemekezeka a Charles Chilambula apereka mabuku ku ofesi yoona za maphunziro m’boma la Likoma.

Pofuna kupititsa patsogolo maphunziro mdziko muno wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo ndi ukhondo yemwenso ndi phungu wa pa zilumba za Likoma ndi Chizumulu wolemekezeka a Charles Chilambula apereka mabuku ku ofesi yoona za maphunziro m’boma la Likoma.

by Chiletso Bisweck
0 comments

Mabukuwa ndi thandizo lochokera ku Malawi National Library Services ngati mayankho pazokambilana zimene mbali ziwirizi zinachita.

Iwo awuza adindo kuti kubwera kwa mabukuwa kuthandiza kulimbikitsa ophunzira chikhalidwe chowerenga.

“Titapempha kuti sukulu zathu zili ndi nyumba zowelengelamo zomwe mulibe mabuku atithandiza ndi mabuku oposa 4,000, omwe athandizire ana athu kukonzekera kokwanira”.

A Chilambula ati atengapo mbali kuti mabukuwa afike m’boma la Likoma polipilira mayendedwe ndi ogwira ntchito kuti mabukuwa afike ku Likoma.

Polandira mabukuwa bwana mkubwa wa boma la Likoma Abubakar Nkhoma ayamikira phunguyu kaamba ka thandizoli ndipo ati mabukuwa afikira sukulu zonse za pulayimale ndi sekondale m’bomali.

Boma la Likoma lili ndi sukulu khumi za pulayimale komanso ma sekondale atatu aboma.

LikomaFM,OnlineNews.

You may also like

Leave a Comment

Likoma (LCR) is a community radio for Likoma District licensed by
Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) in December
2013.The Radio is covering the whole of Likoma District including
Chizumulu, parts of Nkhata Bay,Mzuzu and Nkhotakota. The radio
station enjoys a listenership of about 50,000 comprising of 17,000 from
the island and others from Nkhata Bay, Nkhotakota and some parts
of Mozambique.

Newsletter

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00