Atachita zii kwa zaka zinayi m’modzi mwa oyimba wapa chilumba cha Chizumulu, Memory Pondomali yemwe amatchuka ndi dzina lakuti Nyapondo wati akhala akutulutsa nyimbo yatsopano yomwe akuyitcha “Zani”.
Nyapondo wati nyimboyi yomwe wajambula Video komanso audio zonse zitulutsidwa pa 1 February 2026, “panopa ndikhala okhazikika chifukwa ndinawoloka zomwe zakhala zikundifowoketsa…