Khothi la first grade magistrate ku Likoma lagamula a Kingsley Lamwele a zaka 18 kukakhala kundende ndikukagwila ntchito yakalavula gaga kwa zaka zinayi kaamba kolowa m’nyumba ndi kuba katundu osiyanasiyana.
Malingana ndi oyimira boma pa milandu Sub-Inspector Shallnever Mfune adauza khothili kuti usiku wapa 25 July 2026 odandaulayu adatseka nyumba yake koma…