A Chilambula alankhula izi lero atamaliza kupereka zikalata zawo zowayeneleza kudzapikisana nawo pachisankho chapa 16 September ngati mphungu pansi pa chipani cha Democratic Progressive Party.
“Ndine okondwa kuti ndaloledwa kudzapikisana nawo ngati phungu wa Likoma-Chizumulu Constituency choncho ndikuwapempha omwe analembetsa kuti akavote mwanzeru kuti Likoma wathu apite patsogolo.”
Naye mkulu okopa anthu mchipanichi a Farai Holland ati zatelemu apitiliza kumema anthu okhala m’boma la Likoma kuti adzavotere a Charles Chilambula,
“Nthawi zambiri kulikoma kuno timavotera anthu omwe ndi akuno koma sakhala kuno ndipo amangotiyendera ngati akudzazonda odwala ndikumapita, kulikoma timavutika nkhani yakudula kwa zakudya monga Chimanga, Sugar, ndi mitengo yakuchigayo mwazina koma pa 16 September pano mavuto onsewa akutha.” Atero a Holland.
Pakadali pano bungwe la Malawi Electral Commission, MEC lavomeleza anthu okwana anayi kuti ndiwoyenera kudzapikisana pampando waphungu ku Likoma Constituency, anayiwa ndi a Masauko Thawe oyima pawokha, a Christopher Ashems Songwe a Malawi CongressParty, a Vincent Chirwa a People’s Party, komanso a Charles Chilambula a Democratic Progressive Party.
LikomaFM, OnlineNews.
1 comment