A Chilambula alankhula ndi Likoma radio kuti sanali okhutila ndi chisankho chomwe chinachitika mwezi wa Epulu ndipo ati anthu asamakopeke ndi ndalama koma mfundo.
“takhala tikuyenda pagalawundi ndichimene chandipatsa chitsimikizo kuti kuthekera kutha kupezeka ngati titapanga bwino kampeni”, atero a Philip.
Pakadali pano achilambula akuti chilichonse chofunika kuti adzapikisane nawo apanga kale kuphatikizapo kutenga zipepala ku ofesi ya MEC komanso kupeleka ndalama.
Zatelemu anthu okwana asanu ndiwomwe awonetsa chidwi chodzapikisana pa mpando wa ukhansala mchigawo chakumwela kwa chilumba cha Likoma.
LikomaFM, OnlineNews.