Anthu okhala pa Chilumba cha Chizumulu apempha Boma kuti lipitilize mapulani omanga Jiti pachilumbachi.

Izi zadziwika pa mkumano omwe phungu wanyumba ya malamulo wa Likoma a Christopher Ashems Songwe anayitanitsa adindo osiyanasiyana kuphatikizapo mafumu lero pomwe amapeleka malipoti ake amomwe ntchito za chitukuko zayendera m’bomali kuyambila chaka cha 2019 mpaka 2025.

T.A Kabuthu wa chilumba cha Chizumulu wati zosemphana zomwe zinalipo zokhudza malo omwe jitiyi idzamangidwe zatha tsopano.

Enala Phiri yemwe ndi ochita malonda pa chilumbachi wati amayi ndi achikulire ndiwomwe akuvutika pokwera Sitima ndipo ndipo wati ganizo lopitiliza ntchitoyi ndiyopindulira anthu apachilumbachi

Naye wachinyamata ochokera m’dera la Chiteko pachilumbachi macfallen Mafuta ati ndizoona kuti pakali pano kusemphanaku kunatha ndipo boma lipitilize ndi ganizoli.

LikomaFM, online news.

Related posts

Kampani ya China Civil Engineering Construction kudzera mu unduna wa za mtengatenga ndi mtokoma yapereka ma life jacket 250 ku boma la Likoma.

Wapampando wa khonsolo ya boma la Likoma wati anthu omwe amapindula ndi porogalamu ya mtukula pakhomo adzigwilitsa moyenera ndalama zomwe amalandila mu porogalamuyi.

Gulu la Tilerane la m’mudzi wa mfumu Mani M’boma la Likoma lathandiza mabanja awiri osowa ndikatundu ogonera.