Polankhula lachinayi pamwambo opeleka cement ku komiti yoyendetsa chigayochi, a Innocent Aponda omwe ndi mmodzi mwa guluri ati achita chidwi powona momwe phungu wa Likoma a Christopher Ashems Songwe akuchita pa nkhani ya zitukuko pomwe apeleka zigayo ziwiri dera la Chiponde ndi Chinyanya zomwe azigula ndi ndalama za mthumba mwawo.
Mlembi wakomiti ya chigayochi a Edward Chirwa ayamikira guluri kamba kathandizoli ndipo ati akonza kale ndondomeko yakayendetsedwe kantchitoyi ndipo mwazina ndikuzathandiza osowa, kulipilira feez komanso kukonzera zitukuko zina mdelari.
Mfumu yadelari Group Village Headman Mwase yathokoza a Joe Noel Chilala omwe azayimire delari ngati khansala kamba kosaka thandizoli.
Guluri lapereka matumba okwana khumi.
LikomaFM, OnlineNews.