A Antonio Manda anena izi lero pamkumano omwe amakumana ndi atsogoleri oyendetsa masewero osayinasiyana m’bomali.
M’mawu awo a Manda ati m’boma la Likoma muli zinthu zambiri zofunika kukonza pankhani za masewero, ndipo alonjeza kuti ayesetsa kusaka thandizo m’madera osiyanasiyana ndicholinga chofuna kupititsa masewera osiyanasiyana patsogolo.
“ku Likoma kuli achinyamata omwe ali ndi ma luso osiyanasiyana chomwe chikufunika nchakuti awonekele poyera,” atero a Manda.
M’modzi mwa nthumwi zomwe zinatenga nawo mbali a Raphael Malikita omwe ndi Coordinator kuchoka ku Special Olympics m’bomali ati kusowekela kwa zipangizo ndi ukadaulo wa anziphunzitsi omwe amaphunzitsa masewero osiyanasiyana nkomwe kukupangitsa kuti maluso ena asamaonekere.
Pomaliza a Manda alonjeza kuti masewera omwe atayambe ndi a Beach Soccer ndipo komiti yogwirizila inasinkhidwa kale yomwe wapampando wake ndi a Davie Kacholola.
LilkomaFM, OnlineNews.