Rt.Rev. Fanuel Magangani wanena izi lamulungu lapitali pa St Peters Anglican Cathedral m’boma la likoma pamwambo osangalalira kuti Dioceses yi yakwanitsa zaka 30 ikutumikila.
Amagangani anati mpingo ukuyenela kukhala odzidalira pawokha pachuma osati kumangodali maiko akunja. “kale ngakhale zovala za usembe tinkadalira maiko akunja koma pakadali pano takula chifukwa tikudzipangila tokha”.
Ndipo awonjeza kuti pomwe Dioceses yi yakwanitsa zaka 30 ndiwosangalala kuti yakwanitsa kumanga sukulu komanso zipatala mdziko lino.
Nduna yawona za chitetezo cha mdziko a Ezekiel Ching’oma womwe anali mlendo olemekezeka pamwambowu m’malo mwa president wadziko lino anati boma la Dr Lazarus Chakwela limalimbikitsa kuti mipingo idzigwira ntchito limodzi ndi boma pachitukuko ndipo ndiwokondwa kuti mpingowo ukugwila ntchito yotamandika mdziko.
Dr Lazarus Chakwela wathandiza Dioceses yi ndi ndalama zokwana 10,000,000.00 kwacha, pomwe a Ezekiel Ching’oma anapeleka 5,000,000.00.
LikomaFM, Onlinenews.
1 comment