Ofesi yowona za usodzi ku Likoma yati ndiyokondwa kuti tsopano asodzi ali ndi owaimira ku khonsolo.

Mkulu woyendetsa ntchito za usodzi m’boma la Likoma, Lonjezo Chikopa wati tsopano pakhala posavuta kuti asodzi azitha kutula nkhawa zawo komanso kudziwa zomwe zikuchitika ku khonsolo kutsatila kusankhidwa kwa a Martin Mjima.

A Martin Mjima ati akonzeka kuimilira asodzi pomwe ati m’mbuyomu asodzi akhala akupangilidwa ziganizo popanda iwo eni.

“Tiyamikire khonsolo kamba kaganizoli poti m’mbuyomu tinalibe mpata oterewu,” anatero a Mjima.

Kupatula kukhala oyimira asodzi mnyumbayi a Mjima asankhidwanso kukhala mukomiti ya zaulimi ndi zachuma (Agriculture and finance).

Kusankhidwa kwa mnthumwiyi kukutsatila pempho la khansala wadera la kumwera kwa chilumba cha Likoma Ernest Travor Gulu yemwe anapeleka ganizoli posachedwapa.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Mkulu woyang’anira nkhani za katemera wa Polio mdziko muno, a Blessing Nyirongo ati ali ndi chikhulupiliro kuti kampeni yopeleka katemera wamatendawa m’boma la Likoma ikhala yopambana.

Wamkulu wa kampani ya Malawi Lake Services wati kukweza mitengo kwa sitima ya MV Ilala kupititsa patsogolo ntchito za kampaniyi.

Wapampando oyang’anila chitukuko chadera la kumwera kwa chilumba cha Likoma a Anson Putaputa ati akusowekera maphunziro kuti ayambe kugwira ntchito yawo mwaukadaulo.