Polankhula loweluka pamwambo opeleka katundu kumabanjawa, Wapampando wa Guluri mayi Gladies Njakale ati cholinga chaguluri ndikuonetsetsa kuti anthu akukhala moyo wopanda nkhawa, iwo atinso kuonjezera pakatundu yemwe apeleka lero gulu lawo lipitiliza kugwira ntchito zachifundozi.
Mayi Janet Boma azaka 62 am’mudzi wa mfumu Chilongola mdera la Khuyu omwe apindula ndi thandizori ayamikira gulu la Tilerane chifukwa chathandizoli, ndipo ati ngati nkotheka gululi likachitirenso ena.
Nawo mayi Edina Pitala azaka 83 a m’mudzi wa mfumu Mwase ayamikila gululi ndipo ati thandizoli labwela munthawi yake pomwe tili munyengo yozizira.
Gululi lapeleka bulangete, matres, komanso pilo kwawina aliyense kumabanja awiriwa
LikomaFM, OnlineNews.