Khonsolo ya Boma la Likoma yayamba ntchito yomanga nyumba yosungilamo katundu wa ngozi zogwa mwadzidzi.

Ntchito yomanga nyumbayi yomwe imangidwe ku Ngani pansi pa CHAKO VDC yayambika lero ndipo igwilika kwa masiku 90.

M’mawu awo nkulu oyang’anila ntchito za chitukuko ku khonsolo ya Likoma a Stephen Munthali anati ofesi yawo inasankha pulojekiti yomanga nyumbayi chifukwa boma la Likoma lidalibe nyumba yosungilamo katundu kapena anthu nthawi ya ngozi zogwa mwa dzidzidzi.

“Chitukuko chimenechi chithandiza kwambiri m’boma la Likoma chifukwa si nyumba yongosungilamo katundu yekha. Mwachitsanzo nyumbayi ikhoza kumazagwilitsidwa ntchito ngati sukulu kapena Chipatala pa nthawi yomwe malo oyenerawa aonekeledwa ngozi monga kugwa”, Anatero a Munthali.

Poyankhulapo yemwe anaimila sub T/A Mwase a Bababasi Mkwekweta anati akuthokoza khonsolo ya Likoma chifukwa chosankha chitukuko chimenechi ndipo Iwo ngati eni dela achilandila.

“Taika chikhulupiliro komaso chidwi mwa kontalakita yemwe wapatsidwa ntchitoyi kamba koti aka sikoyamba kupatsidwa ntchito pano pa Likoma, tikuyembekezera kuti agwila ntchito yotamandika momwe anachitila m’mbuyomu”.

Mfumuyi inaonjezera kuti anthu aku delali akhale ndi chidwi pochita kalondolondo pakagwilidwe ka ntchitoyi.

Ndalama zokwana K61,981,145.59 ndizomwe zigwilitsidwe ntchito ndipo thandizoli lachokera ku Bungwe la World Bank.

Ntchito ngati yomweyi ikuyembekezekaso kugwilidwa pa chilumba Cha Chizumulu.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Khonsolo ya Likoma yalandira ma Computer asanu othandizira sukulu ya Likoma community technical college kuchokera ku Bungwe la TEVETA.

Khansala Justina Phiri wa chigawo chakumpoto kwa Chilumba cha Chizumulu ndiyemwe wasankhidwa kukhala Wapampando wa Khonsolo ya Likoma.

11 comments

Colin543 August 6, 2025 - 5:45 am
Catherine53 August 8, 2025 - 10:08 am
Gabriel208 August 8, 2025 - 11:26 am
Carl1186 August 10, 2025 - 1:03 am
Celeste1760 August 16, 2025 - 1:54 am
Frank2038 August 16, 2025 - 6:01 am
Giselle1355 August 16, 2025 - 3:53 pm
Braxton3422 August 16, 2025 - 10:29 pm
Lawrence4533 August 16, 2025 - 11:07 pm
Jolie3223 August 20, 2025 - 10:53 am
Rose4691 August 22, 2025 - 5:58 pm
Add Comment