Kuchedwetsa ntchito kwa kontilakitara kwapangitsa kuti ntchito yomanga chipatala chaching’ono cha YoMa healthy Post m’boma la Likoma chisathe munthawi yake.

Wachiwiri kwa wapampando wakomiti yoyang’anila chitukuko kuderali yemweso ndi wapampando wa chitukuko wa Yoma VDC a Aliston Katemetcha ati kontilakita yemwe akumanga chipatalachi alibe chidwi komanso alibe mantha pa ntchito yomwe anapatsidwa “komiti yoyang’anila ntchitoyi alibe nayo ntchito”, atero a Aliston pomwe anapitiliza kuti akhala akuwapeza ena mwa ogwira ntchito akuzembetsa matumba a cement.

A Aliston alankhula izi lero pomwe khonsolo ya Likoma motsogozedwa ndi mkulu oyendetsa zitukuko mukhonsoloyi anayitanitsa mkumano wadzidzi.

Yemwe anayimila phungu wa Likoma a Mercy ati ngati ofesi ya MP ndi wodandaula kutsatila ndimomwe polojekiti ya Chipatalachi ikuyendela, “dera la Yoma VDC linamapempha chipatalachi kusonyeza kuti anaona vuto ndipo ndi zinthu zopweteka kwa anthu a kuderali kuona chipatala chawo chisakutha mpaka lero”.

A Polera ati chipatalachi chikumangidwa ndi ndalama zochokera mthumba la CDF ndipo a MP anapeleka ndalamazi kalekale ndipo sakudziwa kuti chikuvuta ndichani.

M’mawu ake Director wa Cheyeka Building Contractors a Blessings Ng’oma ati ntchito yawo inakumana ndi mikwingwilima maka pakukwera mitengo kwa zinthu zomwe zinasokoneza ndondomeko yakagulidwe ka zinthu ndipo alonjeza kupitiliza kugwira ntchitoyi kwa masabata anayi.

Chipatalachi chinayamba kumangidwa chaka chatha mwezi wa novembala ndipo chimayenera kutha kwamasiku 90.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Sukulu ya Likoma Sekondale yalandila galimoto ya tsopano yomwe ikhale ikuchepetsa mavuto a mayendedwe.

Bungwe lowona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) litsegulira nyengo ya misonkhano yokopa anthu pa 14 July 2025, pokonzekera chisankho chomwe chidzachitike pa 16 September chaka chino.