A Nyirongo awuza Likoma Radio kuti kupeleka katemelayu kwatengera kupezeka kwa Polio munzinda wa Blantyre kotero a zaumoyo akangalika kupeleka katemelayu komanso kufalitsa mauthenga akuopsa kwa Polio.
Polankhulapo ofalitsa nkhani zaumoyo m’bomali a Adamson Chunga ati ana omwe amalandila katemelayu amakhala otetezeka ku matendawa.
A Chunda ati pali chiyembekezo kuti ntchito yopeleka katemelayu idzayambe pa 24 mpaka pa 27 March 2026, ndipo ana 3644 osaposera zaka khumi zakubadwa ndiwomwe akuyembezeka kulandira katemelayu.