Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwela wapempha achinyamata kuti achite machawi pofusila ndalama ya mthumba la Youth Innovation Fund.

Achakwera anena izi pamsonkhano wa achinyamata omwe ukuchitikira mu mzinda wa Lilongwe pamutu wakuti ‘Harnessing Youth Innovation for Economic Employment and Sustainable Job Creation Towards Malawi 2063’, ndipo ndalama zokwana 2 billion kwacha ndizomwe zapatsidwa kwa achinyamata mu pologalamuyi.

Wapampando wabungwe la Likoma Team Adventure a Yusuf Asima omwe akuchita nawo mkumanowu akuti mkumanowu uwathandizira kwambiri kupititsa patsogolo ntchito yazokopa alendo komanso wapeleka danga pa nkhani zina zomwe achinyamata akuyenera kuchita kuti akwanilitse masomphenya a M2063.

“Kale ndinalibe uthenga okwanila pankhani ya Youth Innovation Fund koma pakadali pano ndadziwa omwe akuyenera kupindula ndi thumba limeneli”, watero Yusuf Asima.

Msonkhanowu unayamba pa 2 July ndipo udzatha pa 4 July 2025.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Sukulu ya Likoma Sekondale yalandila galimoto ya tsopano yomwe ikhale ikuchepetsa mavuto a mayendedwe.

Kuchedwetsa ntchito kwa kontilakitara kwapangitsa kuti ntchito yomanga chipatala chaching’ono cha YoMa healthy Post m’boma la Likoma chisathe munthawi yake.

13 comments

Gabriella2230 August 5, 2025 - 1:27 am
Hector1179 August 5, 2025 - 8:39 am
Evan641 August 7, 2025 - 11:32 am
Tom2254 August 9, 2025 - 9:54 am
Marcel4159 August 12, 2025 - 11:46 pm
Kendall3099 August 13, 2025 - 8:38 am
Mariah649 August 14, 2025 - 7:07 am
Luke1635 August 14, 2025 - 8:16 pm
Payton4958 August 17, 2025 - 1:05 pm
Charlie2783 August 17, 2025 - 3:29 pm
Victor2018 August 17, 2025 - 10:12 pm
Julius1221 August 29, 2025 - 12:03 pm
Luke2268 September 1, 2025 - 3:28 pm
Add Comment