Phunguyu wapeleka thandizo la ndalama zokwana 1,000,000.00-kwacha lachisanu kudzera ku ofesi ya za masewero, District Education Sports Officer (DESO).
Polandila thandizoli mkulu wa za maphunziro m’bomali a Zimulange Mhango ayamikila a Songwe kamba kathandizo lomwe apeleka panthawi yake, ndipo anawonjezera kuti aka sikoyamba kuti Phunguyu athandize pankhani za maphunziro ndi ndalama za m’thumba mwawo, “ulendo wina anathandizira Quiz Competition komanso anyamata omwe ankapita ku mpikisano wa MASSA”, anatero a Mhango.
A Songwe ati ndi khumbo lawo kuona masewero osiyanasiyana akupita patsogolo kudzera m’masukulu chifukwa akudziwa bwino lomwe kuti ana ambiri luso lowe limaonekela akakhala ali pa sukulu, ndipo ati ndichiyembekezo chawo kuti thandizoli ligwira ntchito moyenera.
Thandizoli ladza pomwe ana asanu ndi mmodzi akuyembekezeka kupita ku maiko a Namibia ndi Algeria posachedwapa.
LikomaFM, OnlineNews.