Phungu waboma la Likoma a Christopher Ashems Songwe wati pali zokhoma zina zomwe zachititsa kuti munthawi yawo asakwanitse zina mwa zitukuko zomwe adalonjaza.

A Songwe anena izi lolemba pomwe anakonza mkumano wa adindo osiyanasiyana kuphatikizapo mafumu ndicholinga chowafotokozera zomwe achita kuchokera mchaka cha 2019.

“Munthawi yomwe ndakhala ndikukutumikilani ndakumana ndi zokhoma monga, kufowoka kwa akomiti oyang’anila ma polojekiti akudera, ma komiti a VDC ndi ADC kusalondoloza zitukuko, khonsolo kugula zipangizo zosayenera komanso kuchedwa kuyamba ntchito mwazina” anatero a Songwe.

Komabe phunguyu wati wakwanitsa ena mwa malonjezo ake mwachitsanzo, kubweletsa bwalo lamilandu, kuthetsa mavuto amagetsi, kumaliza zitukuko zimene zinayambidwa kale komanso kukhazikitsa thumba la ndalama zothandizila ana ovutika mu sukulu za sekondale.

Mkumanowu wachitika pomwe ma udindo a aphungu mdziko lino akhale akutha mwezi wa July chaka chino pokonzekela chisankho chapatatu chomwe chidzachitike pa 16 September.

Likomafm, online news.

Related posts

A Charles Chilambula omwe adzapikisane nawo pa mpando waphungu wa nyumba yamalamulo ku Likoma ati apitiliza kuchititsa misonkhano yokopa anthu kuti adzapambane pa chisankho chapa 16 September.

Yemwe adzapikisane nawo pampando wa ukhansala muwodi ya Chizumulu North m’boma la Likoma ati ndiwokonzeka kutumikila anthu akuderali.

A Philip Chika Chilambula omwe anagonja pachisankho chachipulura pa mpando wa ukhansala mchipani cha Democratic Progressive Party DPP, akuti adzapikisana nawo pampandowo ngati oyima pawokha.