Team ya Try Again FC yafika mu ndime yotsiliza mu chikho cha Castel Challenge Cup itagonjetsa Nkhwazi FC 2 kwa du.

Izi zili chonchi kutsatila masewero omwe anachitika Lamulungu lapitali pa Madimba Community Ground mndime ya Semi final pakati pa Nkhwazi fc ndi Try Again fc.

Zigoli ziwiri zomwe Adam Mustapha anamwetsa nzomwe zapangitsa kuti Try Again ifike ndime yotsiliza ndipo anyamata a Nkhwazi fc anakumane ndi kiyama pomwe atuluka wopanda dipo mchikhochi.

Zateremu team ya Try Again FC idzakumana ndi Team ya Chiponde fc mu ndime yotsiliza ya mchikhochi.

Team ya Try Again yafika mundime yotsiliza kachitatu kuchoka momwe chikho cha Castel Cup chinakhazikitsidwa mchaka cha 2023.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Mkulu woyendetsa nkhani za masewero m’boma la Likoma wati anthu okhala m’bomali ayembekezele kuona kusintha pa nkhani za masewero.

Team ya Chiponde FC ndi akatswiri a FAM Cup Under 21 District League itagonjetsa Team ya Red Arrows 4-2.