Yemwe adzapikisane nawo pampando wa ukhansala muwodi ya Chizumulu North m’boma la Likoma ati ndiwokonzeka kutumikila anthu akuderali.

A Andrew Zex Msalowa omwe adzayimile chipani cha Malawi Congress Party MCP, anena izi lero pa Chizumulu Community ground pomwe amakhazikitsa mfundo zawo zokopera anthu kuti adzawasankhe pachisankho chapa 16 September.

A Msalowa akuti anthu akadzawasankha iwo kukhala khansala wadelali adzapititsa patsogolo ntchito zaumoyo, zamaphunziro komanso zamasewero mwazina.

Potsegulira msonkhanowu mdera lachiteko amfumu a Chingole ati ndale simkangano kapena kunyozana ndipo ati atsogoleri omwe akupikisana pamipando yosiyanasiyana ndiwolandilidwa mdelali posatengera chipani.

Polankhulapo wapampando wa amayi kuchigawochi a Grace Mhone apempha anthu kudzavotere a Msalowa kaamba kakuti anayamba kale kupanga zitukuko monga kuthandizila chipatala cha Chiteko under 5 clinic ndi matumba a cement komanso lime mwazina.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

A Charles Chilambula omwe adzapikisane nawo pa mpando waphungu wa nyumba yamalamulo ku Likoma ati apitiliza kuchititsa misonkhano yokopa anthu kuti adzapambane pa chisankho chapa 16 September.

A Philip Chika Chilambula omwe anagonja pachisankho chachipulura pa mpando wa ukhansala mchipani cha Democratic Progressive Party DPP, akuti adzapikisana nawo pampandowo ngati oyima pawokha.

Phungu wa boma la Likoma a Christopher Ashems Songwe apeleka thandizo ku ofesi ya maphunziro m’bomali kuti lithandizile masewero osambila.

1 comment

Coraline2335 August 5, 2025 - 1:27 am
Add Comment