Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwanyengo yati nyengo ya Chiperoni ikuyembekezeka kuchepa mphanvu lero ndipo mawa m’madera ambiri kudzakhala kwa nyengo ya dzuwa, koma mvula idzagwa m’madera ochepa am’chigawo chakumpoto.Nthambiyi ikupitiliza kuchenjeza asodzi kupewa kulowa pa nyanja pogwilitsa ntchito mabwato ang’ono ang’ono munthayi.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Mkulu woyang’anira nkhani za katemera wa Polio mdziko muno, a Blessing Nyirongo ati ali ndi chikhulupiliro kuti kampeni yopeleka katemera wamatendawa m’boma la Likoma ikhala yopambana.

Wamkulu wa kampani ya Malawi Lake Services wati kukweza mitengo kwa sitima ya MV Ilala kupititsa patsogolo ntchito za kampaniyi.

Ofesi yowona za usodzi ku Likoma yati ndiyokondwa kuti tsopano asodzi ali ndi owaimira ku khonsolo.