Likoma FM
  • Home
  • Featured
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Lifestyle
  • Sports
  • About Us
  • Contact
  • Login
  • Likoma FM

    Khothi la first grade magistrate ku Likoma lagamula a Kingsley Lamwele a zaka 18 kukakhala kundende ndikukagwila ntchito yakalavula gaga kwa zaka zinayi kaamba kolowa m’nyumba ndi kuba katundu osiyanasiyana.

    Apolisi m’boma la Likoma amanga a Charlse Banda, powaganizira kuti anachita chipongwe msungwana wazaka khumi.

    Mkulu woyang’anira nkhani za katemera wa Polio mdziko muno, a Blessing Nyirongo ati ali ndi chikhulupiliro kuti kampeni yopeleka katemera wamatendawa m’boma la Likoma ikhala yopambana.

    Kuchedwetsa ntchito kwa kontilakitara kwapangitsa kuti ntchito yomanga chipatala chaching’ono cha YoMa healthy Post m’boma la Likoma chisathe munthawi yake.

    Chiletso BisweckJuly 22, 20250440 views

    Wachiwiri kwa wapampando wakomiti yoyang’anila chitukuko kuderali yemweso ndi wapampando wa chitukuko wa Yoma VDC a Aliston Katemetcha ati kontilakita yemwe akumanga…

    Read more

    A Philip Chika Chilambula omwe anagonja pachisankho chachipulura pa mpando wa ukhansala mchipani cha Democratic Progressive Party DPP, akuti adzapikisana nawo pampandowo ngati oyima pawokha.

    Chiletso BisweckJuly 12, 20250357 views

    A Chilambula alankhula ndi Likoma radio kuti sanali okhutila ndi chisankho chomwe chinachitika mwezi wa Epulu ndipo ati anthu asamakopeke ndi ndalama…

    Read more

    Bungwe lowona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) litsegulira nyengo ya misonkhano yokopa anthu pa 14 July 2025, pokonzekera chisankho chomwe chidzachitike pa 16 September chaka chino.

    Chiletso BisweckJuly 12, 20250398 views

    Malingana ndi kalata yomwe bungweri ladatulutsa pa 9 Julayi ndipo wasaina ndi mneneri wa bungweri a Sangwani Mwafulirwa yati mwambo otsegulira nyengo…

    Read more

    Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwela wapempha achinyamata kuti achite machawi pofusila ndalama ya mthumba la Youth Innovation Fund.

    Chiletso BisweckJuly 3, 202513724 views

    Achakwera anena izi pamsonkhano wa achinyamata omwe ukuchitikira mu mzinda wa Lilongwe pamutu wakuti ‘Harnessing Youth Innovation for Economic Employment and Sustainable…

    Read more

    Khonsolo ya Boma la Likoma yayamba ntchito yomanga nyumba yosungilamo katundu wa ngozi zogwa mwadzidzi.

    Chiletso BisweckJune 9, 202511707 views

    Ntchito yomanga nyumbayi yomwe imangidwe ku Ngani pansi pa CHAKO VDC yayambika lero ndipo igwilika kwa masiku 90. M’mawu awo nkulu oyang’anila…

    Read more

    Bishop wa Anglican Dioceses of Northern Malawi wati mpingo uli ndi udindo waukulu potengapo mbali pachitukuko chadziko lino.

    Chiletso BisweckJune 3, 202510456 views

    Rt.Rev. Fanuel Magangani wanena izi lamulungu lapitali pa St Peters Anglican Cathedral m’boma la likoma pamwambo osangalalira kuti Dioceses yi yakwanitsa zaka…

    Read more

    Phungu wa boma la Likoma a Christopher Ashems Songwe apeleka thandizo ku ofesi ya maphunziro m’bomali kuti lithandizile masewero osambila.

    Chiletso BisweckMay 31, 20250371 views

    Phunguyu wapeleka thandizo la ndalama zokwana 1,000,000.00-kwacha lachisanu kudzera ku ofesi ya za masewero, District Education Sports Officer (DESO). Polandila thandizoli mkulu…

    Read more

    Gulu la Taskforce lomwe ndi nthambi ya chipani cha Malawi Congress Party m’boma la Likoma lapeleka Cement kuti amalizile nyumba ya chigayo.

    Oliver MalibisaMay 22, 20250337 views

    Polankhula lachinayi pamwambo opeleka cement ku komiti yoyendetsa chigayochi, a Innocent Aponda omwe ndi mmodzi mwa guluri ati achita chidwi powona momwe…

    Read more

    Wapampando wa khonsolo ya boma la Likoma wati anthu omwe amapindula ndi porogalamu ya mtukula pakhomo adzigwilitsa moyenera ndalama zomwe amalandila mu porogalamuyi.

    Chiletso BisweckMay 18, 20250391 views

    A Barnabas Sambamu anena izi lamulungu pomwe khonsolo ya Likoma inakonza masewelo ampira wamiyendo ndicholinga chakuti apeleke uthenga wamomwe porogalamuyi imayendela, pamutu…

    Read more

    Gulu la Tilerane la m’mudzi wa mfumu Mani M’boma la Likoma lathandiza mabanja awiri osowa ndikatundu ogonera.

    Oliver MalibisaMay 10, 20250501 views

    Polankhula loweluka pamwambo opeleka katundu kumabanjawa, Wapampando wa Guluri mayi Gladies Njakale ati cholinga chaguluri ndikuonetsetsa kuti anthu akukhala moyo wopanda nkhawa,…

    Read more

    Posts navigation

    1 … 3 … 5
    View Desktop Version

    Powered by PenciDesign

    Back To Top