Malingana ndi mneneri wa Police ya Likoma a Andrew Kusimbwa ati kumangidwaku kwachitika pambuyo pa ntchito yomwe inachitika ndi a polisiwa.
“A Banda atiuza kuti anamuuza mwanayo kuti awagwire kumaliseche kwawo, koma mwanayo anakana”
“Iwo akuti anachita zimenezi potsatira malangizo a sing’anga, pokhulupirira kuti mchitidwewu ungamupange kukhala wolemera”, watero Kusimbwa.
A Kusimbwa ati mwanayo anapulumutsidwa ndi amayi ake, omwe anapita kukamufunafuna ataona kuti sanabwerere kunyumba kutsatila kuyitanidwa ndi oganilizidwayu, ndipo amayiwa atafika kunyumba kwa a Banda anapeza zitseko zonse zotsekedwa koma anamva mawu a mwana wawo akufuula kuti athandizidwe.
A Charlse Banda amachokera m’mudzi wa mfumu Mtaya, T.A Mkhumpha m’boma la Likoma ali ndizaka 39 akawonekera kukhoti kuti akayankhe mlandu wochitala mwana zachipongwe.