Bungwe lowona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) litsegulira nyengo ya misonkhano yokopa anthu pa 14 July 2025, pokonzekera chisankho chomwe chidzachitike pa 16 September chaka chino.

Malingana ndi kalata yomwe bungweri ladatulutsa pa 9 Julayi ndipo wasaina ndi mneneri wa bungweri a Sangwani Mwafulirwa yati mwambo otsegulira nyengo ya misonkhano ya kampeniyi udzachitikila mu mzinda wa Lilongwe.

Bungweri lati liyitana oyimila zipani, nthambi zaboma komanso mabungwe oyima pawokha mwa ena, ndipo apempha anthu onse kudzatsatira mwambowu kudzera mnyumba zowulutsa mau ndipo Likoma Community Radio idzakupatsilani tsatanetsatane wa mwambowu kuyambila 9 koloko m’mawa.

Pofika lero atsogoleri okwana 17 ndiwomwe awonetsa chidwi chodzapikisana nawo pampando wa President.

LikomaFM, Online News.

Related posts

Sukulu ya Likoma Sekondale yalandila galimoto ya tsopano yomwe ikhale ikuchepetsa mavuto a mayendedwe.

Kuchedwetsa ntchito kwa kontilakitara kwapangitsa kuti ntchito yomanga chipatala chaching’ono cha YoMa healthy Post m’boma la Likoma chisathe munthawi yake.