Wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo yemwenso ndi phungu wa Likoma Islands Constituency a Charles Chilambula ati kubwera kwa incinerator m’boma la Likoma kupititsa patsogolo ntchito za umoyo.

A Chilambula anena izi lamulungu kutsatila kufika kwa incinerator yi pa chipatala cha Chima m’bomali.

“Kumbuyoku tikafuna kuwotcha zinthu zina tinkazitumiza ku St Gabriel koma tsopano vutoli lichepa”, anena choncho a Chilambula.

Iwo awonjezera kuti tsopano zinthu zidziwotchedwa munthawi yake zomwe zichepetse kufala kwa matenda omwe amadza kudzera mu mpweya oyipa.

Polankhulapo bwana mkubwa wa boma la Likoma Abubakar Nkhoma ayamikira wachiwiri kwa ndunayi pothandizira kuti makinawa afike ku Likoma ndipo ati tsopano ndalama zomwe khonsoloyi inkagwilitsa ntchito powotchera zinyalala kuntunda zidzigwira ntchito zina.

Malingana ndi a Chilambula pakadali pano incinerator ngati imeneyi ili mu mzinda wa Mzuzu ndi boma la Likoma mchigawo cha kumpoto kwa dziko lino.

LikomaFM,OnlineNews.

Related posts

Khothi la first grade magistrate ku Likoma lagamula a Kingsley Lamwele a zaka 18 kukakhala kundende ndikukagwila ntchito yakalavula gaga kwa zaka zinayi kaamba kolowa m’nyumba ndi kuba katundu osiyanasiyana.

Apolisi m’boma la Likoma amanga a Charlse Banda, powaganizira kuti anachita chipongwe msungwana wazaka khumi.

Wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo yemwenso ndi phungu wa Likoma Islands Constituency olemekezeka a Charles Broomhead Chilambula ati boma ndilodzipereka kupititsa patsogolo ntchito zaumoyo.