Pofuna kupititsa patsogolo ntchito za Maphunziro m’dziko muno, Nduna ya Maphunziro a Madalitso Kambauwa Wirima atsegulira ofesi ya aphunzitsi (TDC) pa chilumba cha Chizumulu m’boma la Likoma.

Polankhula la chiwiri pa Chilumba cha Chizumulu pamwambo otsegulira ofesiyi omwe unatsogozedwa ndi Phungu wa Likoma a Christopher Ashems Songwe, ndunayi yati ntchito za maphunziro zimayenda bwino aphunzitsi akakhala ndi Malo abwino komanso zipangizo zokwanila, ndunayi yatinso ntchito yomanga Laboratory yomwe pakadali pano ilinkati pachilumbachi ikhala ikutha posachedwapa.

Polandila ofisiyi mkulu oyendetsa maphunziro musukulu za primary pachilumba cha Chizumulu a Macdonald Kondowe ati ofesiyi ichepetsa mavuto omwe analipo kaamba kakuti ankagwilitsa kalasi yophunziliramo.

“tsopano makalasi omwe anali ma ofesi aphunzitsi abwezeledwa kwa ana”. Atero a Kondowe.

Naye phungu wa Likoma a Christopher Ashems Songwe wayamika utsogoleri wa Dr Lazarus Chakwera kamba Ka Zitukuko zomwe zikumangidwa ku Likoma ndipo wapemphanso undunawu kuti uganizire aphunzitsi a m’bomali powakweza mawudindo komanso Boat lomwe lingamathandizire pamavuto omwe Sukulu ya Sekondale ya Likoma ikukumana nawo.

Ndalama zokwana K115,152,508.21 zochokela muthumba la GESD ndizomwe agwilitsa ntchito pomanga ofisiyi.

Itatsegulira ofesiyi ndunayi inakayendera Sukulu ya Likoma sekondale komwe yalonjeza kuti Boma likhala likuyamba kukonza sukuluyi posachedwa kuti iwoneke mwamakono

LikomaFM, Online News.

Related posts

Sukulu ya Likoma Sekondale yalandila galimoto ya tsopano yomwe ikhale ikuchepetsa mavuto a mayendedwe.

Kuchedwetsa ntchito kwa kontilakitara kwapangitsa kuti ntchito yomanga chipatala chaching’ono cha YoMa healthy Post m’boma la Likoma chisathe munthawi yake.