Pomwe dziko lino likukonzekera chisankho chapatatu bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electral Commission likupitiliza kudziwitsa adindo osiyanasiyana za ndondomeko yachisankho.

Mkulu owona zachisankho m’boma la Likoma a Theophilus Msachi lero achititsa mkumano wa mafumu ndi atsogoleli azipembedzo pofuna kuwadziwitsa za ntchito yotsimikizila maina mukaundula wazisankho yomwe ichitike posachedwapa.

“Timafuna tiwapemphe mafumu komanso atsogolire azipembedzo potengela kuti anthu amenewa amakhala ndi mwayi okumana ndi anthu ambiri panthawi imodzi, ndipo ife a MEC sitingathe kukumana ndi aliyense payekhapayekha” atero a Msachi.

A Msachi ati okhawo omwe analembetsa mukaundula wachisankho ndiomwe akufunika kudzapita ku senta yomwe analembetsela kaundula wachisankho kakatsimikiza maina awo ndipo ngati pali zolakwika zina adzathandizidwa panthawi komanso omwe chaphaso chawo chovotera chinasowa adzapatsidwa china.

Mlembi wa atsogolire azipembedzo a Gift Manda ati mkumanowu wachitika munthawi yake ndipo ati ndi udindo wawo kulimbikitsa nzika za dziko lino kuti zikatsimikize maina awo panthawiyi.

Boma la Likoma lili mugawo lachiwili wa kaundulayu yemwe achitike kuyambila pa 21 mpaka 23 May, 2025.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Sukulu ya Likoma Sekondale yalandila galimoto ya tsopano yomwe ikhale ikuchepetsa mavuto a mayendedwe.

Kuchedwetsa ntchito kwa kontilakitara kwapangitsa kuti ntchito yomanga chipatala chaching’ono cha YoMa healthy Post m’boma la Likoma chisathe munthawi yake.