Wamkulu wa kampani ya Malawi Lake Services wati kukweza mitengo kwa sitima ya MV Ilala kupititsa patsogolo ntchito za kampaniyi.

A Joseph Sheketani Banda alankhula izi lachinayi pamkumano omwe anakonzera atolankhani a m’boma la Likoma ndicholinga chowadziwitsa momwe kampaniyi imagwilira ntchito zake.

Iwo ati kampaniyi imadziwa bwino lomwe kuti anthu okhala m’boma la Likoma amadalira sitima ya MV Ilala.

“M’mene timayendera pa ulendo wathu amene amayifunitsitsa sitima ya Ilala ndi anthu okhala ku Likoma, choncho tikakhazikitsa ubale wabwino ndi inu atolankhani anthu akulikoma adzinva uthenga wathu mwamsanga”, atero a Banda.

Iwo ati paulendo umodzi sitima ya MV Ilala imafunikira 35 Million Kwacha kuti agule mafuta komanso zakudya za ogwila ntchito ndipo kukweza kwamtengowu kuthandizira kuti sitimayi idziyenda munthawi yake.

A Banda atinso kuchokera pa 1 May 2025, pomwe boma linayamba kuyendetsa kampaniyi makampani ena awonetsa kale chidwi chothandiza kampaniyi pogula sitima zamakono kaamba kakuti MV Ilala ndiyakale.

Polankhulapo m’neneri wa khonsolo ya Likoma Ireen Mseteka wati mkumanowu wathandizira kuti adzifalitsa uthenga oyenera wa kampaniyi.

Malingana ndi a Banda, pakadali pano sitima ya MV Ilala imapanga pafupifupi 60 Million Malawi Kwacha pa ulendo umodzi pomwe m’mbuyomu ulendo ngati omwewu inkapanga 5 Million kwacha yokha basi.

LikomaFM,OnlineNews.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Mkulu woyang’anira nkhani za katemera wa Polio mdziko muno, a Blessing Nyirongo ati ali ndi chikhulupiliro kuti kampeni yopeleka katemera wamatendawa m’boma la Likoma ikhala yopambana.

Ofesi yowona za usodzi ku Likoma yati ndiyokondwa kuti tsopano asodzi ali ndi owaimira ku khonsolo.

Wapampando oyang’anila chitukuko chadera la kumwera kwa chilumba cha Likoma a Anson Putaputa ati akusowekera maphunziro kuti ayambe kugwira ntchito yawo mwaukadaulo.