Vuto lakusowa kwa madzi a ukhondo lafika posauzana pa chilumba cha chizumulu m’boma la Likoma.

Polankhula ndi Likoma Radio mkulu woyang’anira sikimu ya Chizumulu water users Association (Chiuwa) a Sikele Longwe ati pakadali pano athedwa nzeru kaamba ka vuto la kubowoka kwa ma lift pump komanso vuto la Mota zomwe zikupangitsa kuti asamapope madzi.

Iwo ati ayesetsa kugogoda ku khonsolo ya Likoma kudzera ku ofesi ya madzi kuti athandizepo pa vutoli koma palibe chomwe yachitikapo.

“tinapemphaso kwa anzathu a Northern Region Water Board nawonso sanatiyankhebe kufikila lero.”

A Longwe ati ndalama zomwe amatolela pa mwezi sizimaposa 1.5 million kwacha zomwe ndizochepa kuyendetsera sikimuyi.

Koma a Longwe ati sikimu yawo simadula madzi kwa ma kasitomala awo omwe adutsitsa nthawi yopeleka ma bill chifukwa chakuti akawadulira madzi amakatunga kunyanja.

Naye wapampando wa komiti yoyang’anila chitukuko chakudera (ADC), a Mwayi Chirwa ati komiti yawo yakhala ikukambilana zavutoli ku mikumano yake koma sakupeza yankho.

“panopa tikumakhala masiku anayi nthawi zina sabata opanda madzi a ukhondo.” Atero a Chirwa.

LikomaFM,OnlineNews.

Related posts

Sukulu ya Likoma Sekondale yalandila galimoto ya tsopano yomwe ikhale ikuchepetsa mavuto a mayendedwe.

Kuchedwetsa ntchito kwa kontilakitara kwapangitsa kuti ntchito yomanga chipatala chaching’ono cha YoMa healthy Post m’boma la Likoma chisathe munthawi yake.

Bungwe lowona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) litsegulira nyengo ya misonkhano yokopa anthu pa 14 July 2025, pokonzekera chisankho chomwe chidzachitike pa 16 September chaka chino.