Apolice M’boma la Likoma agwira abambo atatu ndikuwasunga muchitolokosi powaganizira mulandu wakuba komanso kupezeka ndi katundu wa anthu omwe anamira pangozi ya bwato yomwe inachitika loweluka sabata yapitayi m’bomali pomwe anthuwa amakakwera sitima ya MV Chilembwe.
Malingana ndi ofalitsa nkhani za Police ku Likoma sergeant Enala Kaluwa wati pawukadaulo wawo akwanitsa kugwira anthuwa ndipo onsewa akuyembekezeka kukawonekera kubwalo…