Apolice M’boma la Likoma agwira abambo atatu ndikuwasunga muchitolokosi powaganizira mulandu wakuba komanso kupezeka ndi katundu wa anthu omwe anamira pangozi ya bwato yomwe inachitika loweluka sabata yapitayi m’bomali pomwe anthuwa amakakwera sitima ya MV Chilembwe.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za Police ku Likoma sergeant Enala Kaluwa wati pawukadaulo wawo akwanitsa kugwira anthuwa ndipo onsewa akuyembekezeka kukawonekera kubwalo la mulandu posachedwapa pa mlandu opezeka ndi katundu wakuba.

Atatuwa ndi a Sunganani soko
azaka 31 am’mudzi wa Chioko, T.A Nkumpha boma Likoma. Nyangana Nyasulu azaka 32 am’mudzi wa Matandani, T.A Kamwandi boma la Nkhatabay, ndi a Chisomo Ganizani azaka 26 am’mudzi wa Kosamu, T.A Njombwa boma la Kasungu.

Kaluwa wati akwanitsanso kugwira m’modzi mwa anthu omwe amayendetsa bwato lomwe linanyamula anthuwa omwe anamila.

Related posts

Khothi la first grade magistrate ku Likoma lagamula a Kingsley Lamwele a zaka 18 kukakhala kundende ndikukagwila ntchito yakalavula gaga kwa zaka zinayi kaamba kolowa m’nyumba ndi kuba katundu osiyanasiyana.

Apolisi m’boma la Likoma amanga a Charlse Banda, powaganizira kuti anachita chipongwe msungwana wazaka khumi.

Wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo yemwenso ndi phungu wa Likoma Islands Constituency a Charles Chilambula ati kubwera kwa incinerator m’boma la Likoma kupititsa patsogolo ntchito za umoyo.