Ofesi yowona za usodzi ku Likoma yati ndiyokondwa kuti tsopano asodzi ali ndi owaimira ku khonsolo.

Mkulu woyendetsa ntchito za usodzi m’boma la Likoma, Lonjezo Chikopa wati tsopano pakhala posavuta kuti asodzi azitha kutula nkhawa zawo komanso kudziwa zomwe zikuchitika ku khonsolo kutsatila kusankhidwa kwa a Martin Mjima.

A Martin Mjima ati akonzeka kuimilira asodzi pomwe ati m’mbuyomu asodzi akhala akupangilidwa ziganizo popanda iwo eni.

“Tiyamikire khonsolo kamba kaganizoli poti m’mbuyomu tinalibe mpata oterewu,” anatero a Mjima.

Kupatula kukhala oyimira asodzi mnyumbayi a Mjima asankhidwanso kukhala mukomiti ya zaulimi ndi zachuma (Agriculture and finance).

Kusankhidwa kwa mnthumwiyi kukutsatila pempho la khansala wadera la kumwera kwa chilumba cha Likoma Ernest Travor Gulu yemwe anapeleka ganizoli posachedwapa.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Wapampando oyang’anila chitukuko chadera la kumwera kwa chilumba cha Likoma a Anson Putaputa ati akusowekera maphunziro kuti ayambe kugwira ntchito yawo mwaukadaulo.

Khonsolo ya Likoma yalandira ma Computer asanu othandizira sukulu ya Likoma community technical college kuchokera ku Bungwe la TEVETA.

Khansala Justina Phiri wa chigawo chakumpoto kwa Chilumba cha Chizumulu ndiyemwe wasankhidwa kukhala Wapampando wa Khonsolo ya Likoma.